Prepared by Mr Katimba (0888606823)
KUDZUKUTA NDAKATULO ZA A BENEDICTO WOKOMAATANI
MALUNGA, M`BUKU LA
“KUIMBA KWA MLAKATULI”
MUTU WOYAMBA
Kodi ndakatulo ndi chiyani?
Ndakatulo ndi maganizo opekedwa mwachidule ndipo amayalidw m`ndime kapena
mopanda ndime.
Ndakatulo zimapekedwa pamitu yosiyanasiyana monga chikondi, chilengedwe,
umodzi, kudalirana, umbava, nkhanza, ulamuliro, maphunziro, chisoni,
chisangalalo ndi zina.
Kufunika kwa ndakatulo
Ndakatulo ndizofunika kwambiri pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku chifukwa
zimaphunzitsa, zimasangalatsa, zimadziwitsa, zimachenjedza, kuyamikira ndi
kutonthonza.
Mitundu ya ndakatulo
Ndakatulo zimaikidwa m`mitundu molingana ndi magwero ake. pali mitundu
yambiri ya ndakatulo monga zotsatirazi:
Ndakatulo zodandaula (chisoni)
Ndakatulo zachisangalalo
Ndakatulo zodzudzudzula
Ndakatulo zoyamikira
Ndakatulo zogalukira
1
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
Kayalidwe ka ndakatulo
Ndakatulo zimayalidwe potsatira imodzi mwa njira izi
MAPASA (mu ndime)
MPULULIRA (mopanda ndime)
Popeza gwero la ndakatulo ndi nyimbo, ndakatulo zina zitha kuimbidwa ndi
zomwe zimayalidwa mwa dongosolo. kutalika kwa mizere yandakatulo zomwe
zitha kuimbidwa kumakhala kwa dongosolo potsata chiwerengero cha maphatikizo
a mawu opanga mzera.
CHITSANZO
NDIWE MKOKERI WACHISUMPHI SIDA
Ndiwedi wachisumphi mkokeri mtengo wa sida
Wokulenga mwatsankho, padziko adakuponya
Kulebabanoni mthaka nakuokera mwadumbo wokoo!
Mulanje m`Malawi mthaka nakuthibwiliza eti
Poti mombo, msanya, malaina, m`bawa ya khalila nsanje akuchitira kaamba ka
chako chodabwitsa chilengedwe.
Ndiwedi mkokeri wachisumphi sida
Ndiwe namwali olondeledwa ndi amfuti asilikali iwe uligone! uko kumapiri,
poti okulikha aseweza yakalavulagaga
jere amaumau akawanyonga, ndiwedi njanji
2
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
ya aluminium padenga lofoleledwa mwaluso
ndiwedi mtengo wotininkha lupiya wokusamala akakuchengeta bwino
tandiyankhe mafunso otsatirawa mwanawe sida
mchifukwa ninji umapezeka maiko awiri okha padziko lapansi?
Nanga maokeraokera, poti umachita dumi, umakaniranji ngakhale yachanjira
nthaka?
Nanga tandiulilira mwanawe, chiswe, agan`ga komanso abembelizu amachitiranji
chidzungulira akakunyambita?
Ndiwedi mkokeri wachisumphi mtengo wa sida.
(YOPERKEDWA NDI VINNIE KATIMBA)
ZIPANGIZO ZA CHICHEWA M`NDAKATULO
CHIBWEREZA CHA MAU: awa ndi mau amene amatchulidwa koposa kamodzi
m`ndime iliyonse ngakhale m`ndakatulo za m`pululira cholinga chosendera
komanso kusindika mfundo.
MAU OMVEKA MOFANANA KUMATHERO WA MZERE M`NDIME
KAPENA MKALEMBEDWE KA MPULULIRA: awa ndi mau amene
akatchullidwa amamveka mofanana ngakhale tanthauzo limasiyana. nthwi zambiri
mau amenewa amalembedwa kumathero kwa ndime ndizo izi zimaonesera luso
komanso ukadaulo wa mlembi.
WOYANKHULA: uyu ndi munthu kapena chinthu chomwe chikuchita zinthu
m`ndakatulo
3
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
WOYANKHULIDWA: munthu kapena chinthu chomwe chikuchitidwa zinthu
m`ndakatulo.
MALO NDI NTHAWI: Uku ndikomwe nkhani yam`ndakatulo ikuchitikira. Malo
ndi nthawi itha kukhala nthawi zenizeni kapena nyengo. pamene mukuzukuta
ndakatulo perekani umboni wogwirika otsimikizira za malo ndi nthawi zomwe
mwatchula.
TANTHAUZO/MEANING: Pali mitundu iwiri ya matanthauzo
(i) Tanthauzo lobisika/lakuya (deeper meaning)
Ili ndi tanthauzo limene mlembi walifotokoza mobisa. nthawi zina
amayankhula (Mosipa). Kuyankhula zachinthu china chodziwika pamene
tanthauzo lenileni akufotokoza za munthu kapena chinthu chosiyana.
(ii) Tanthauzo lachindunji (surface meaning)
Ili ndi tanthauzo limene mlembi amalipereka mowonekera komanso
mwachindunji. Ngati akufotokoza kapena kukamba za msinje, tanthauzo
silimasintha.
CHIYANKHULO NDI NSETSO
Alakatuli ambiri monga bamboo Malunga amasankha mau mwaluso. choncho
pamene mukudzukuta ndakatulo fotokozani zamsinjiroza chiyankhulo komanso
mau apadera omwe wopeka ndakatulo wagwiritsa ntchito.
Pamene mukudzukuta ndakatulo, fotokozani momveka bwino momwe mlakatuli
wagwiritsa ntchito zipangizo monga izi: mpeputso, mafunso achodziwadziwa,
chifanifani, voko, chidzindikiritso, chifaniziro, kulowana kwa mau, kasinira mau,
kalamikiza komanso mtsinjiro za mchiyankhulo.
4
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
CHITHUNZITHUNZI
Chithunzithunzi ndi chinthu chomwe womvera kapena wowerenga
nkhani/ndakatulo amachiona kapena kuchimva m`maganizo mwake.
chithunzithunzi chimakhuza zinthu monga zotsatirazi:
(a)kuona ndi maso
(b)kumva m`makutu
© kukhuza pakhungu
(d)kumva pathupi
(e)kumva m`mphuno (fungo)
(f) kumva palilime (kakomedwe)
Komanso kuyenda kapena kugwedeza thupi.
MUTU WACHIWIRI
KUIMBA KWA MLAKATULI
(1) ALEKENI AGUNDUNGU.
(Benedicto Wokomaatani Malunga)
5
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
*ndakatulo yamapasa (ya ndime)
UTHENGA WAUKULU(MFUNDO)
Ikukamba za anthu ansanje, kaduka komanso dumbo amene mtima wawo
umatupa mnzawo akamachita bwino. amakondwera mnzawo akagwera
m`mavuto osiyanasiyana.
Anthu otere amakhala olephera, ukawasiyira ntchito kuti agwire sakwanitsa
ngakhale amachita nsanje. kufooka kapena kubwerera m`mbuyo kaamba ka
anthu ansanje ndikusowa masomphenya.
MATANTHAUZO A MAWU MCHINYANJA CHOMWE MLEMBI
WAGWIRITSA NTCHITO
Mbuto = malo
Kuwereweta = kulalata
Chisimo = chidzolowezi
Dambizi = kaduka(nsanje)
Kusambwaza = kunyoza
Kushodola = kujeda
Akalakambombo = anthu opanda pache
ZIPANGIZO ZINA ZOSINJIRA CHINYANJA M`NDAKATULO
(i) CHINYANJA CHOBWANDIRA CHIDWI CHA AWERENGI
“Mukasunthira pena poti ndoto, kukhosi, kumayenda nkhono”.
“mukadumphira apo ndi khamulo tulo limawathera”
(akaona pena kumva kuti zikukuyendera amadwala ndi msanje)
CHIFANIZIRO
Mlembi wayelekedzera zinthu zosiyanasiyana kuyesesa kufotokozera kuipa/kuopsa
kwa msanje. lichikhala lisilo kaduka linali losamva sopo.
6
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
Lichikhala matenda linali losamva mankhwala.
KUTANURA MALINGALIRO
Kupitabe patsogolo zokukokerani m`mbuyo nzambiri. mlembi wayerekezera
ulendo wapanjinga yakapalasa pokwaritsa masomphenya.
“njinga nayo kutha mtunda, kutchova umo mungatheremo gwetsani mapiri
mnjiramo, salazani zitunda m`malunjemo poti m`mbalimo mulibe icho
mwakhumbacho”
MTSINJIRO ZINA ZACHIYANKHULO.
Moyo si use anka kwakuntha mphepo, mwiniwe mchiongolero
((osamayendetsedwa ndi maganizo a ena. mwiniwe panga ziganizo zoyendetsera
moyo wako))
WOYANKHULA: Munthu kapena mlangizi (namkungwi) yemwe amadziwa
bwino kuipa komvera mabodza komanso anthu opandapache.
WOYANKHULIDWA: akhonza kukhala ophunzira yemwe ena akumunena kuti
akuchedwa ndi sukulu. kapena wochita malonda kapena munthu yemwe
wasankhidwa udindo pakati pawanthu ena omwe sakondwera.
PHUNZIRO: Zomva kuphweteketsa mutu. sibwino kuyang`ana m`mbali pamene
ukuchita zinthu zomwe wazisankha.
7
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
AMAYI AWA
Ndakatulo ya mapasa (ya ndime)
MFUNDO YAIKULU (UTHENGA)
Mndakatulo ikukamba za amayi ambiri achimalawi omwe amalimbikisa kuchita
malonda mkumathandiza ana komanso mabanja awo.
MAWU ACHILENDO NDI MATANTHAUZO AKE POTENGERA NDI
MOMWE MLEMBI WAWAGWIRISIRA NTCHITO.
Thungwa =Lichero laling`ono
Kuthyakula = kuphika nsima (kusakaniza ndi ufa)
Mfutso = ndiwo za masamba zoumisa/kusunga
Nanyati = mtundu wanyemba
Chipilinganye = kusakaniza bwino
Amanda =mtundu wa mpunga
Zikanyanga =zimphwa
Malasankhuli =zombe (bwamnoni)
ZIPANGIZO ZINA MCHINYANJA ZIMENE MLAKATULI WABWANDIRA
NAZO CHIDWI CHA AWERENGI
“Ngumbi zomwe akagwira nzokodolera ndalama”
“amayi awa sukulu itawalambalala makezana”
8
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
“phiri lansima yokodolo manja wonjenjemera ndi nyala. Awaamanda odzutsa
Amanda” =mau omveka mofanana(ryming)
CHIFANIZIRO
Mlembi wafanidzira kulimbikira komanso kuchitachita kwa amayi
akukambidwawa monga zinthu izi:
(i) Njuchi
(ii) Nyerere
MALO NDI NTHAWI
Mlakatuli m`ndakatuloyi akuyamika amayi aku malwi makamaka
wachita chidwi ndi amayi ochokera m`malo otsatirawa:
(i) Lizulu
(ii) Mlangeni
KUTANURA MALINGALIRO PAMFUNDO YAIKULU
M`NDAKATULO
Amayi amene sukulu idawavuta kalelawo koma salabadira zofooka
zamoyo wawo pochilimika m`kuchita malonda mpaka kuphunzitsa
ana omwe lero ndi nzika zodalilika kuno kwathu ku Malawi, ngati
adaphunzira kuchokera mubizinesi yaing`ono ngati anyezi,
kachewere, ngumbi ngakhalenso ndiwo zamasamba.
WOYANKHULA: Munthu (atha kukhala mwamuna) amene wachita chidwi ndi
kulimbika komanso kukangalika kwa amayi pamalonda.
WOYANKHULIDWA: Amayi onse achimalawi amene amachita malonda
mkumathandiza mabanja awo.
PHUNZIRO: Ukaipa dziwa nyimbo
9
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
Amayi amene alibe kuthekera kopeza ntchito chifukwa sukulu idawavuta
akukwanitsa kuchita zambiri m`moyo kaamba kolimbika pochita malonda.
3. ANKALOTA NDANI
Ndakatulo ya mpululira (yopanda ndime)
MFUNDO YAIKULU (UTHENGA)
Mlembi akuyamikira mmene anthu komanso dziko likupindulira kuchokera
kumaluso osiyanasiyana amene poyamba sankanunkha kanthu.
MAWU ACHILENDO NDI CHINYANJA CHINA CHIMENE MLEMBI
WAGWIRITSA NTCHITO
“Luso nkukhala mbale yodyera”
(ena mkumakhala m`moyo wa tsiku ndi tsiku kudalira luso)
“chikopa atadyanacho wani kuopa thupi kupindika”
(Akuchita bwino kaamba kampira ndipo ali poyambilira)
Anamatetule = akatswiri
Dziko posukusula = dziko podzindikira makono ano.
KUTANURA MALINGALIRO PA MFUNDO YAIKULU M`NDAKATULOYI
Luso lomwe lidali lopanda pache poyamba makono ano lasanduka chida chomwe
chikupindulira ena lero ngakhalenso Dziko. Mlembi wasilira, alakatuli azitsunzo,
osewera mpira, oimba ngakhalenso atolankhani amene akutukuka, kutchuka
ngakhale mmaiko ena, kuzidalira paokha chifukwa cha luso lawo.
10
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
MALO NDI NTHAWI
Mlembi wapeleka chitsanzo cha agiriki komanso ku Roma kumene zidayambira
ntchito za luso asadafotokoze zakuno kwathu kumalawi.
WOYANKHULA munthu yemwe wachita chidwi ndi momwe luso
likutukulira anthu komanso dziko makono ano.
WOYANKHULIDWA munthuyu ndi chidwi chake akudziyankhulira yekha.
PHUNZIRO Chinenepetsa nkhumba sichidziwika. Nkwabwino kulimbikira
zinthu zimene umadzikwanitsa ngakhale mzonyozeka.
ANZANU AKUKUWA
Ndakatulo ya Mapasa (yandime)
MFUNDO YAIKULU (UTHENGA)
Mlembi akufotokoza oyo woipa wa anthu ogundana nyumba maka mmatuwni (ma
neighbours) pokhala chete komanso kusadziwitsa apolisi pamene mnzake akuba
amfuti (aupandu afika pakhomo)
CHINYANJA NDI MAU OBWANDIRA CHIDWI CHA AWERENGI
“Anzanu akuona zakuda zoyera zili khale” (Akuona mavuto)
“Mmawa kutacha inu buli m’nyumba” (kulawirapo osakaona ana)
MVEKERO Mipeni ili waliwali
Zisenga zili chezichezi
Mpungwepungwe utafumbira (zitafika pampondachimera/povuta)
Mantha powatafuna ngati manu chingamu (pochotsa mantha)
KUTANURA MALINGALIRO MOZAMA PA MFUNDO YAIKULU
M’NDAKATULO
11
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
Woyankhulayu akuyamika Mutu wa banja (mwamuna) wake kaamba kakulimba
mtima komanso ukaziotche pa nthawi imene amaliongo adafika mnyumba
mwawo. Mayi woyankhulayi akuyamikiranso ana ake pa umodzi wawo polimbana
ndi a Maumau opanda chisoni makmaka mwana wake wa mwamuna yemwe
adaonetsera kuti adatengera bamboo wake ukadziotche pothandizana nawo mpaka
kugonjetsa ambanda.
Atalephera kuchitapo kanthu a neighbour mwamuna adalimba mtima mkugonjesa
ambanda
CHIFANIZIRO
Mlembi wafanidzira mantha ndi chinyamu komanso ukaziotche wa amuna ake
monga kambuku.
“Osaka atasnduka osakidwa m’malunje poti kuchuluka sikunaphule kanthu koma
cholinga cha chauta”
Mlembi akuna mphamvu ya chauta kudzera mwa mwamuna wake amene wa
tsogolera kuombola banja lake m’mavuto oopsa.
WOYANKHULA: Mayi yemwe kunyumba kwake kudabwera ambanda ochuluka
kufuna kuzaba komanso kuwononga.
WOYANKHULIDWA: Mayiyu akuzilankhulira yekha popukwa zones zomwe
zidachitika pa tsiku losaiwalikali.
PHUNZIRO: Mnzako akapsa ndevu mzimire, ndibwino kuthandizana pamene
anzanthu akumana ndi mavuto
BWERERANI
Ndakatulo ya mapasa (yandime)
MFUNDO YAIKULU (UTHENGA)
12
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
Woyankhula ndi munthu wachikulire amene amaona chibwana komanso kunyada
kwa achinyamata ambiri mmene amanyozera ulimi, kukhala kumudzi akaphunzira.
CHINYANJA CHOBWANDIRA MOYO
“Mgaiwa wachikalaya atakumera “(atakukola/atakukwana)
“Akupha mkonono (kugona) pakama ogula yekha”
“zomulora ngati zamulawulo (zokolola zamuyanja)
KUTANURA MAGANIZO PA UTHENGA MNDAKATULO
Woyankhulidwa ndi achinyamata onyada amene akuchita manyazi kubwelera
kumudzi pamene akuvutika mtawuni kaamba sadachoke bwino paja m’mbuyo
mwabwino Mtsogolonso mwabwino.
Woyankhulidwayu akutsonyeza chidwi maka powauza achinyamata kuti azizalima
monga momwe achitira anzawo Gamalieli komanso Yokoniya amene adazichepesa
kumalima mwaukadailo kumudzi ngakhale adapita ku sukulu mokwanira choncho
chifukwa cholimbika zinthu zikuwayendera.
KWANU NKWANU MTHENGO MUDALAKA NJOKA
Mlembi watsimikizira mau awa maka poonetsera machokedwe a achinyamata ena
amene amachita mwano akaphunzira mkumatsilira ntchito zapamwamba komanso
kunyoza kumudzi.
PHUNZIRO: Fodya wako ndiwaphuno wapachala ngwamphepo; osanyoza kapena
kupeputsa chinthu chimene utachichita ndi khama chikupindulira ndi kuthamangira
zina zimene zimaoneka zabwino koma zili kutali.
13
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
CHAKANA CHAKANA
Ndakatulo ya mpululira (yopanda ndime)
MFUNDO YAIKULU (UTHENGA)
Mlembi akufotokoza za anthu osalabadira zowawa zomwe ena amamva maka
powalimbikitsa kuti azipilira pamene iwo eni ali mumtendere.
WOYANKHULA Angakhale mwana wamkazi yemwe akuchitidwa nkhanza koma
akulu akumulimbikitsa kuti asaulure. Woyankhulayu akudzilankhulira yekha.
MAU MCHINYANJA CHIMENE MLEMBI WABWANDIRA NACHO
CHIDWI CHA AWERENGI
“Ndizitsekelera chomwa madzi ometera” (chitsiru, choipa)
“ndinachilozera yakwao njira ndi muni” (ndidamthamangitsa)
CHIFANIZIRO
Mlembi wafanizira zinthu zosiyanasiyana ndi nkhanza/mavuto omwe akukumana
ndi mkazi
I. Wafanizira chitupsa chakupsa
II. Dzino lobola
III. Goli
IV. Kulumidwa
V. Chibekete chosasunga madzi
M’ndakatloyi mlembi wagwiritsa ntchito luso pofotokoza mobisa
uthenga weniweni omwe akupereka kwa awerengi.
KUTANURA MAGANIZO PAUTHENGA OMWE MLEMBI
AKUSANTHULA M’NDAKATULO.
Mkazi walolera kunenedwa komanso kutonzedwa koma
kuthamangitsa/kupitikitsa chimwamuna cha nkhanza chopanda pake kuti
bola apezeko mtendere.
14
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
PHUNZIRO: Chakanachakana dazi lilibe mankhwala. Sibwino
kukakamira zinthu zomwe zikutibweretsera mavuto kuti tisangalatse ena.
CHIBWANA CHA MCHOMBO LENDE
Ndakatulo yampululira (yopanda ndime)
UTHENGA WAUKULU (MFUNDO YOFUNIKIRA)
KAFIKENI BWINO
Ndakatulo ya mpululira (yopanda ndime)
UTHENGA WENIWENI MWACHINDUNJI
Mlembe wafotokoza mwaluso za munthu (mlendo) amene ali ku dziko lachilendo
kutali zedi ndipo akupuka (kukumbuka za kwao) pamene akutsanzika.
MAFUNSO ACHODZIWADZIWA
Awa ndi mafunso amene woyankhula wafunsa pamene ankaziyankhulira.
i. Kodi kuli mweziko nkutali chotani?
ii. Nanga wondiyankhulayo wabisala pati?
iii. Uchilindekhawu nkupitilira bwanji pagombe pano?
iv. Nanga nkhwawira za miluluzi nkukafika nazo kuli abale anga?
Kufunsa mafunso amene mayankho ake ndi achidziwikire kumasonyeza
kudzingwa kapena kusimidwa ndi nyengo yomwe munthu akudutsa.
ZINTHU ZACHILENDO ZOMWE WOKUMANA NAZO KUDZIKO LA
CHILENDO
*akukhala pagombe pamene uchindeka (kukhala yekha kwamukwana)
15
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
*kuli anthu ozikonda kuopsa kwa maonekedwe a dzikolo
Woyankhulayu wakumbukira mowa owawa umene kwao (komwe
akupitaku) amachita kulandizana poyelekedza ndi (muliyenda) kuchilendo
kumene uchindekha wamukwana. Gamazulu (mowa owawa) amamwa
pochotsa nkhawa
MVEKERO
Mlembi wagwiritsa ntchito mvekero zosiyanasiyana ngati zipangizo
potsinjira Chichewa maka pofuna kupereka uthenga wake mwaluso.
*maso akati thaa kuthambo
KUTANURA MALINGALIRO PA UTHENGA WOMWE MLEMBI
WAPEREKA MNDAKATULOYI
Woyankhulayu wapukwa chikwalidwe chakwawo kumene anthu amakhala
mokondwera ngakhale amasowa zofunikira m’moyo poyerekedzera ndi ku
chilendo komwe aliku kumene akudya bwino (mandazi) koma anthu ake
sacheledza alendo. (“nanga wondiyankhulayo wabisala pati?”)
PHUNZIRO: kwanunkwanu mthengo mudalaka njoka. *zinthu za chilendo,
zokoma komanso zosangalatsa mmoyo sizipangitsa kuti munthu aiwale
kwawo.
KOMWE ALENGA CHIKONDIKO
UTHENGA WAUKULU
Woyankhula mndakatuloyi akuyamikira luso la mulungu polenga mkazi
wokongola kwambiri komanso modolora moyo.
ZINTHU ZOMWE WOYANKHULA WAZIYAMIKA MWA MKAZIYU
*magodi (mabowi ang’onoang’ono m’masaya) omwe akuulula kukongola kwa
nkhope yosalalayo
*mayendedwe
*kayankhulidwe
16
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
*mavinidwe
*mavalidwe
Mlembi wafanizira chilengedwe ndi nyumba yotsungiramo katundu wochitira
umisili (warehouse)
Mnyumba imeneyi malingana ndi malingaliro a mlembi mkomwe kumapezeka;
*chikondi
*chimvano
*ndi mbuto ya magodi
*matupi okoma
*komwe amawa tsitsi
*asoka zovala zapamwamba
Ndikomweko komwe kumapezeka (kumachokera) NDUKE (mkazi okongola
kolapitsa)
ZINTHU ZOMWE ZIMAMCHITIKIRA MWAMUNAYU POMWE MKAZIYU
AKUDUTSA
a) Maso amasusukira kumuwona (kukubwira)
b) Mtima umachita phakuphaku (sukhazikika)
c) Tulo timasowa
Ndukeyi idavumbuluka kuchokera ku (warehouse) ngati mtsinje wotsika
kumapiri ndi madzi wotsitsimusa moyo.
KUTANURA MALINGALIRO PA UTHENGA MNDAKATULO
Chikondi chibweretsa chimvano, maonekedwe abwino komanso
kuzisamalira kubweretsa mudyo maka poyamikira luso ndi kuzama kwa
Namalenga pa chilengedwe chake.
PHUNZIRO: Chikondi
17
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
KUDIKIRA NTHAWI
Ndakatulo ya Mpululira (yopanda ndime)
UTHENGA WAUKULU
Woyankhula akuwakumbusa anthu OIPA pazonse zoipa zomwe amachita padziko
pano kuti likudza tsiku la chiweruzo limene iwo adzakhala akufunsidwa pa zonse
akhala akuchitira ena.
CHINYANJA CHOMWE MLEMBI WAGWIRITSA NTCHITO POFOTOKERA
BWINO UTHENGA WAKE
*LIpenga loutsa ogona ku misitu yachete (lousa anthu akufa)
*lozambafusa mkafe wongofooka nkhongono (lousa onse ongogona
mwachibwana)
*mukachiyambalala kuti chinyanja chodzitetezera maondo akuombana (mau
odzitchinjiriza muzawapeza kuti mukunjenjemera)
ZINA MWA ZIKHALIDWE ZOIPA ZIMENE MLEMBI WAZITCHULA
MNDAKATULOYI
*Kuyankhula monyoza komanso motumbwa
*kuba ana mkukawagulitsa kudziko lakutali
*kupha mwa nkhanza
*ufiti (umthakati)
Mlembi wafotokozera bwino kuti anthu onse ochita zoterezi amatero chifukwa
chofuna kusangalasa owatuma, kufuna mphamvu ndi ulamuliro, chuma komanso
chisangalalo.
KUTANURA MALINGALIRO PA UTHENGA MNDAKATULOYI
Tsiku la chiweruzo lidzadza modzidzimutsa maka pa onse omwe akuchita zoipa.
Mapiri amafunso adzachuluka ngakhale pano sangavomeleze koma kusangalatsa
owatumawo.
18
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
Podzitama anthu oipa amanyoza Namalenga ndi kuiwalira charango chomwe chili
kudza.
PHUNZIRO: KUKONZEKERA; monga momwe mbala imadza mwini nyumba ali
mkafe nkofunikanso anthu ankomzekere kuzayankha milandu yosiyanasiyana
patsiku loopsa lomwe lili kudza
Ukatambatamba udziyang’ana kunyanja kungakuchere.
KUKADA KWADA
Ndakatulo ya Mpululira (yopanda ndime)
UTHENGA WAUKULU
Mlembi/woyankhula akukumbuka ngozi ya madzi Napolo Ku Phalombe.ndipo
akudziyankhulira yekha.
CHINYANJA CHOBWANDIRA MOYO CHOMWE MLEMBI WAGWIRITSA
NTCHITO
*Tsiku la bwinobwino posanzika (mmene kukada madzuro)
*michesi povala ndiwira ya makungwa (mapiri pofunda mtambo wamvula)
*misinje inadzimbidwa (inakhuta/kudzadza madzi)
KUTANULA MALINGALIRO
Mitengo yachilengedwe monga tsanya komanso mombo zidathothoka ngati
zotsalimba, miyala yakalekale idadzuka monga yofewa, anthu adafera ku tulo
komanso nyama poti madzi oopsa adafika usiku.
MALO NDI NTHAWI
Ndakatuloyi ikufotokoza za Ngozi ya madzi a Napolo yomwe idapha anthu, nyama
komanso kusintha maonekedwe a Boma la Phalombe popeza madzi ankadutsa apo
pamene akufuna.
Mlembi akuulula za ngoziyi maka poyerekera za momwe anthu ankayembekezera
zobwera ndi nyengo ya dzinja.
19
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
Anthu aku phalombe ankayembekezera kuti mvula ibweretsa Chimwemwe maka
pothandizira mmera monga chimanga, mpunga komanso kudzadza kwa mtsinje wa
Phalombe.
PHUNZIRO: Chakudza sichiyimba ng’oma.
KUDIKIRA NTHAWI
Ndakatuloyi ndi yamapasa (yandime)
UTHENGA WAUKULU
Mlembi akufotokoza komanso kudandaula za kuphedwa kwa anthu atatu andale ku
Thambani. Anthuwa adali Amatenje, a Gadama komanso a Chiwanga. Iwo
adaphedwa nthawi ya ulamuliro wachipani chimodzi.
KUTANULA MALINGALIRO AMLEMBI
Mlembi akudzudzulanso anthu adachita izi ponena kuti ngakhale iwo sadadziwike
mulungu akuwadziwa ndipo adzawaimba mlandu patsiku la chiweruzo. Mlembi
akuti zonsezi zikudikira nthawi basi.
MFUNDO ZAZIKULU
1. NKHANZA: kuphedwa kwa anthu kukuulura nkhanza zomwe
ulamuliro wa chipani chimodzi udali nazo.
2. KUGWIRITSA NTCHITO UDINDO MOLAKWIKA: Poteteza
maudindo anthu ena ankalolera kupha onse otsutsana nawo.
3. KUSALOLERANA: Kulephera kulolera zomwe ena atilangiza
ngakhale tingadzindikire kuti ndi zoona.
ZIPANGIZO ZOMWE MLEMBI WAGWIRITSA NTCHITO
Zining’a:
Kugwira mtengo
Ndipsi (mbava)
Kuledzera ndi udindo
20
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
CHICHEWA CHOBWANDILA MOYO M’NDAKATULO
Lowetsa ku misitu kwa chete. (kupha)
Kuledzera ndi maudindo
Mapiri amafunso akukudikirani. (mafunso ochuluka)
MVEKERO
Neng’a
Thaa
Mbuu
MAWU A CHILENDO
Dumbo= kaduka, msanje
Liwombo= pakati pamutu
Mmalunje= mngolowera/mthengo
Nyundo= hamara
PHUNZIRO
Pansi pathambo palibe chinsinsi
MADYADO AMAGULE
Ndakatulo ya mapasa (ya ndime)
MFUNDO YAIKULU
Ndakatuloyi ikukamba za magule osiyanasiyana omwe a Malawi amavina malinga
ndi chikhalidwe chawo, Angoni(ingoma), Achewa (beni), Ayawo (manganje),
Alomwe (tchopa) ndi Achewa (gulewamkulu)
21
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
MATANTHAUZO A MAWU ENA
Dzinthu = zokolora
Chilembwe = mtundu wagule wamkulu
Fuko =mtundu wa anthu mdziko
Ng’oma = mtundu wagulewamkulu
Kuwedza kudziwe = kubwera kwa gulewamkulu kuchokera kumanda
ZIPANGIZO ZOMWE MLEMBI WAGWIRITSA NTCHITO
M’NDAKATULOYI
Umunthu: mikondo ikumwa m’manja
Chining’a: chilembwe ng’oma
PHUNZIRO
Kusunga chikhalidwe kumaonesera kukonda fuko komanso dziko
NDAMENEWA MAYI WANGA
Ndakatulo ya mpululira (yopanda ndime)
MFUNDO YAIKULU
Woyankhula ndi mwamuna, iye akuwonetsa mkazi kwa amayi ake ndipo
akumuuzanso zambiri yake.
Woyankhulayu bamboo ake adamwalira.
MFUNDO ZAZIKULU
1. CHIKONDI
Woyankhula ali pachikondi ndi mkazi amene akumuwonesera kwa
amayi ake.
Mayi ake a woyankhula awonetsa chikondi pollera mwana wawo
okhaokha atamwalira amuna awo
2. IMFA
Bambo ake a woyankhula adamwalira iye asadakule kwambiri
22
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
ZIPANGIZO ZOMWE MLEMBI WAGWIRITSA NTCHITO
UMUNTHU
Ukalamba pomanga ufumu pa iwo
Shire watikodolayu
ZINING’A
Akalozera a Maluzi kumasoko =makwinya aukalamba
MKULUWIKO
Wakwatiwa ndi kumbuyo komwe
PHUNZIRO
Kukumbukira chikondi cha omwe adatilera maka pamene takula komanso
kutukuka
NDAONA KAROTI
Ndakatuloyi ndi ya mpululira (yopanda ndime)
Woyankhula akuyamikira kukongola komanso chikhalidwe cha mkazi. Zina mwa
zomwe zakopa mtima wa woyankhulayu ndi izi:
Kuledza mtima
Ulemu
Wovala modzilemekeza
Wosatengeka ndi za dziko
Wozisunga osati wachimasomaso
MFUNDO ZAZIKULU
1) CHIKONDI
23
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
Mnyamata wagwa m’chikondi ndi mtsikana wokongola mmaonekedwe
komanso mchikhalidwe
2) KUYAMIKIRA
Mnyamata akuyamikira kukongola kwa mtsikana
ZIPANGIZO ZIMENE MLEMBI WAGWIRITSA NTCHITO
i. CHIFANIZIRO
Kufanizira mawonekedwe a mtsikana ndi chipaso (KAROTI) kusalala
(nyenje za chimanga)
ii. ZINING’A
Ndawona karoti (ndawona mkazi okongola)
Kukana zogwa mchiswe (kukana amuna achisawawa)
iii. ZIFANIFANI
Mawere oti njo ngati mphonda
Tsitsi ngati nyenje za chimanga
CHICHEWA CHOBWANDIRA MOYO KWA AWERENGI
Amalume anga tambala atakumbatira
Kukodwa m’chikondi monga diwa, mbeta zichitira m’dzanja la msodzi
komanso lauzimba
Miyendo yopopedwa bwino (miyendo yaikulu)
Makono ndauma (ndakalama)
Moto waunyamata (mphamvu za unyamata)
MATANTHAUZO A MAWU ENA
Mphambe = chauta, mlengi
Magodi = timaenje tam’masaya (dimples)
Tsitsi lamzindo = losalala, lachonde mwachilengedwe
PHUNZIRO
Chikondi choloza maonekedwe komanso chikhalidwe
24
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
NKHALAMBA
Ndakatulo ya mapasa (ya ndime)
UTHENGA WA M’NDAKATULO
Kholo lokalamba likudandaula chifukwa mwana wake sakumulabadira. Mwanayu
chipitilireni ku ntchito salemba kalata komanso kutumiza chithandizo
Woyankhulayu ali pa umphawi waukulu
Akugona m’nyumba yothonya komanso ya utitili
Matenda sachoka mthupi kotero kuti akusowa thandizo la mankhwala
MFUNDO ZAZIKULU
I. CHIKONDI
Ngakhale nkhalambayi sikusamalidwa komabe ikufuna kumva za
moyo wa mwana wake ndipo iye akhala okondwa kumva kuti ali
bwino.
II. NKHANZA/KUSALABADIRA
Woyankhulidwayu ndi mwana wa nkhanza komanso odzikonda.
Waiwala mwansanga thandizo komanso chikondi chimene kholo lake
lidapereka kwa iye.
III. UMPHAWI
Umphawi ukuonetsedwa pamene kholo likugona m’nyumba yodontha
komanso ya utitili. Khololi likuvutika ndi matenda osiyanasiyana
posowa thandizo la mankhwala komanso likuvala sanza.
ZIPANGIZO ZIMENE MLEMBI WAGWIRITSA NTCHITO
a) M’BISO (IRONY)
Imwani
25
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
Idyani
Sangalalani
b) MAFUNSO ACHODZIWADZIWA
Nanga ichi chikhale chifukwa chondisalira ngati ndine wakhate?
A chimwene ndikakalamba nde mundiiwale?
PHUNZIRO
Mako ndi mako angachepe mwendo.
Kwanunkwanu mthengo mudalaka njoka
NYIMBO YA CHIKONDI
Ndakatulo ya mpululira (yopanda ndime)
MFUNDO YAIKULU
Woyankhula akuyamikira kukongola kwa mkazi. Mnyamatayu watekeseka
kopambana kotero kuti akumuuza mkazi zinthu zopatsa chiyembekezo.
ZINTHU ZOMWE ZADOLORA MOYO WOYANKHULAYU
Magodi (dimples)
Nkhope yosalala
Tsitsi lamzindo
MFUNDO ZIKULUZIKULU
a. CHIKONDI
Woyankhulayu wagwa m’chikondi ndi woyankhulidwa yemwe ndi
mkazi wokongola kwambiri.
ZIPANGIZO ZOMWE MLEMBI WAGWIRITSA NTCHITO
26
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
MVEKERO
Nyivu
CHIFANIFANI
Chikondi chokuludzanitsani kwa ine ngati mlatho
MAFUNSO ACHODZIWADZIWA
Kodi Nanzare ya chikondi mkukhala makhuma otere?
Nanga mbuto yachisangalalo kubwera kwake mkotero?
UCHINGOFOTOKOZA
Ndakatulo ya mpululira (yopanda ndime)
Mwamuna wadabwa ndi kusintha kwa mkazi wake mmaonekedwe, khalidwe
komanso mayankhulidwe.
Nabiyeni (woyankhulayu mkazi wake) akuganizira mwamuna wake kuti
ngosakhulupilika choncho asadafunse wangosintha nzochitika
MFUNDO ZIKULUZIKULU
A. KUIPA KOSAMASUKIRANA
Mkazi akumukaikira mwamuna wake koma sakufunsa kapena
kukambirana
ZIPANGIZO ZOMWE MLEMBI WAGWIRITSA NTCHITO
CHIFANIFANI
Wakuda bii ngati mdzodzo
MKULUWIKO
Munthu salakwira mtengo
CHINING’A
27
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
Chibwana chamchombo lende
MVEKERO
Bibibi
UMUNTHU
Si misonzi chitambaya chikamayamwa
PHUNZIRO
Kukambirana kumadzetsa mtendere
Zakumva kupweteketsa mutu.
Mawu ochokera kwa Mr Katimba: maphunziro ndi chuma chosalandidwa ndi
akuchimuna.
THE END
28
Prepared by Mr Katimba (0888606823)
29