0% found this document useful (0 votes)
85 views

Chichewa II

This document is a mock examination paper for the Chichewa subject as part of the 2023 Malawi School Certificate of Education in Chiradzulu District. It includes instructions for answering questions across various sections, including language rules, comprehension, and summarization. The paper also features a reading passage followed by comprehension questions and a summary task.

Uploaded by

saizifabiano54
Copyright
© © All Rights Reserved
We take content rights seriously. If you suspect this is your content, claim it here.
Available Formats
Download as PDF, TXT or read online on Scribd

You are on page 1/ 11

DZINA: _________________________________ SUKULU: ___________________________

CHIRADZULU DISTRICT
2023 MALAWI SCHOOL CERTIFICATE OF EDUCATION MOCK EXAMINATION

CHICHEWA

Subject Number: M032/II

Monday, 27 March Time Allowed: 2hrs

11: 30-1: 30 pm

PAPER II

(Malikisi 90)

Malangizo:

1. Onetsetsani kuti pepalali lili ndi masamba khumi Funso Chongani Muno
ndi limodzi. funso ngati musalembemo
2. M’gawo A: Malamulo a Chiyankhulo: Yankhani mwayankha
mafunso onse. (Malikisi 40)
1
2
3. M’gawo B: Kumvetsa Nkhani: Yankhani mafunso 3
onse. (Malikisi 20) 4
4. M’gawo C: Chifupikitso. (Malikisi 15) 5
5. M’gawo D: Kumasulira nkhani (Malikisi 15)
6
7
6. Lembani dzina lanu ndi sukulu pamwamba pa
tsamba lililonse loyankhirapo. TOTAL
7. Muchitebulo chili pamwambachi onetsani funso
lililonse lomwe mwayankha pochonga mubokosi
lomwe lili kutsogolo kwake.

1
DZINA: _________________________________ SUKULU: ___________________________

Gawo A (Malikisi 40)

Malamulo a Chiyankhulo

Langizo: Yankhani mafunso onse.

1. a. Kodi maina otsatirawa adachokera ku ziyankhulo ziti?

(i) sumbulere ___________________________________(Malikisi 1)

(ii) zenera ___________________________________(Malikisi 1)

(iii) muti __________________________________ (Malikisi 1)

b. Kodi aperekezi omwe adulidwa mzere m’ziganizo zotsatirazi akugwira ntchito yanji?

(i) Iye anabwera pa ndege.

______________________________________________ (Malikisi 1)

(ii) Musamadule mitengo m’mbali mwa mtsinje.

______________________________________________ (Malikisi 1)

(iii) Ukatsikire pa Nkando.

____________________________________________ (Malikis 1)

c. Lembani chitsanzo chimodzi cha mifuwu yomwe ingagwire ntchito izi:

(i) Kusonyeza kukondwa ___________________________________________
(ii) Kusonyeza kudabwa ___________________________________________
(iii) Kusnyeza kunyansidwa ___________________________________________
(iv) Kusonyeza kulira _____________________________________________
(Malikisi 4)

2. a. Perekani mitundu ya alumikizi omwe atsekedwa mzere kunsi kwawo

m’ziganizo zotsatirazi.

2
DZINA: _________________________________ SUKULU: ___________________________

i. Poti mwatero, ndipita.

________________________________________________ (Malikisi 1)

ii. Sankawerenga choncho walephera mayeso.

________________________________________________ (Malikisi 1)
iii. Mundigulire malaya osati nsapato.
________________________________________________ (Malikisi 1)
iv. Ine ndadya ndipo ndakhuta.
________________________________________________ (Malikisi 1)

b. Lembani ziganizo zomveka bwino zomwe zikhale ndi “ndi” yemwe agwire ntchito
zotsatirazi ndipo mudule mzere kunsi kwa” ndi.”

(i) Kukhala mneni wodalira

______________________________________________________________
____________________________________________ (Malikisi 2)
(ii) Kukhala mgwirizanitsi
______________________________________________________________
____________________________________________ (Malikisi 2)

(iii) Kukhala mvekero

______________________________________________________________
____________________________________________ (Malikisi 2)

3. a. Tchulani kanenedwe ka aneni omwe atsekedwa mzere kunsi kwawo m’ziganizo

zotsatirazi.

3
DZINA: _________________________________ SUKULU: ___________________________

(i) Maliya wamenya mwana.

_____________________________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) Ndipite nanu kumsika.
_____________________________________________________________
(Malikisi 1)
(iii) Ndikupatsa ukafuna.
_____________________________________________________________
(Malikisi 1)
(iv) Ndabwera kuti mundione.
___________________________________________________________
(Malikisi 1)
b. Lembani mitundu ya akapandamneni omwe adulidwa mzere kunsi kwawo.
(i) Yohane ndi ochenjera ngati kalulu.
____________________________________________________ (Malikis 1)
(i) Mwana wanga wamkazi wabwera.
_________________________________________________ (Malikisi 1)

c. Perekani matanthauzo awiri osiyana a nseketso zotsatirazi:

(i) Nsima yavala jekete.

1. ___________________________________________________________

2. ________________________________________________________

(Malikisi 2)

(ii) Yeremia ndi kapitawo.

1. ______________________________________________________
2. ______________________________________________________
(Malikisi 2)

4
DZINA: _________________________________ SUKULU: ___________________________

4. a. Lembani ziganizo zomveka bwino ndi mimvekero ya mitundu yotsatirayi ndipo

mutseke mzere kunsi kwa mvekerowo.
(i) Mvekero wamakhalidwe
__________________________________________________________________
______________________________________________
(Malikisi 2)
(ii) Mvekero wamamvekedwe
__________________________________________________________________
______________________________________________ (Malikisi 2)
b. Sankhani nthambi zosaima pazokha m’ziganizo zotsatirazi ndipo mutchule
mtundu ndi ntchito zawo:

(i) Mwatengazo ndi zakuba.

1. Nthambi yosaima payokha:
____________________________________________
2. Mtundu:
____________________________________________
3. Ntchito:
___________________________________________ (Malikisi 3)
(ii) Izi ndi zomwe umafuna.
1. Nthambi yosaima payokha:
_____________________________________________
2. Mtundu:
_____________________________________________
3. Ntchito:
_____________________________________________ (Malikisi 3)

Gawo B (Malikisi 20)

Kumvetsa Nkhani ndi Kusanthula Chiyankhulo

5
DZINA: _________________________________ SUKULU: ___________________________

5. Werengani nkhani ili m’munsimu ndipo muyankhe mafunso otsatirawo.

WAKUFA SADZIWIKA

Munthu akakhala wonenepa, wamtali ndi wozuka amatha kudererera mnzake yemwe ali
wochepa thupi ndiponso wamfupi poganiza kuti alibe mphamvu. Koma choyenera kudziwa
n’chakuti mwamuna mnzako m’pachulu, umalinga utakwerapo. Izitu sinkhambakamwa chabe
ayi, mnzanune ndidaziona m’mudzi mwa Tsikula.

A Moya adali munthu wamtali bwino, wakuda. Adali bambo wojintcha zedi ndipo powaona
aliyense amamvetsa kuti apa pagona anthu. Tsiku lina malinga ndi kusowa kwa nkhuni iwo
adapala moto kudambwe. Iwo adakalowa m’munda mwa bambo Fatsani kukadula mtengo
womwe udali wouma bwino. A Moya sadasamale zokapempha chilolezo kwa mwini mundayo.
Chifukwa chake chidali chachidziwikire. Amadziyetsa amphamvu zedi poyerekeza ndi a
Fatsani, eti pongoona maonekedwe. Iwo sanazindikire kuti maonekedwe amapusitsa.

A Moya adagundika kudula mtengo m’munda muja uku akuyimba nyimbo osalabadira zoti
m’mundamo simunali mwawo. Ali pakati posanja nkhunizo kuti amange mitolo, a Fatsani
adatulukira ali pefupefu, diso lili pamtunda. Akuyandikira pa malopo, iwo adati, “Ndiwe yani
ukusimbwa m’munda mwanga?”

Posawugwira mtima a Moya adayankha, “ Ndine Moya, ukuti bwanji?”

“Tsopano chikatere?” Adafunsa a Fatsani atagwira manja m’chiuno.

Posafuna kusisima, a Moya adati, “Sukuona kuti ndimadula mtengo ndipo tsopano ndikulongeza
nkhunizi kuti ndizipita kumudzi?” Izitu amayankha mtima uli zii. Zoti zimene amachitazo kudali
kulakwa sizidawakhuze m’pang’ono pomwe. Mopsa mtima a Fatsani adanenetsa kuti mtengo
womwe a Moya adadulawo udali wawo. Pachifukwa ichi adati, “Nkhunizi simutenga
achimwene. Mukadakhala ena mukadapempha kaye musanadule mtengowu.”

Pamene paja padabuka mkangano waukulu zedi. Anthu ena odutsa m’njira adayamba kubwera
pafupi kuti adzamve chomwe chidautsa mapiri pa chigwa. Ena adayetsetsa kuwathandiza
maganizo a Moya. Anthuwo adati chidali chinthu chopambana kugonja popeza iwo adalakwadi

6
DZINA: _________________________________ SUKULU: ___________________________

pokalowa m’munda mwa mwini wopanda chilolezo. A Moya sanagwirike. Adanenetsa kuti
nkhunizo sakanazisiya ndipo ngati idali ndewu ikhalapodi ya fumbi kobo!

Adanena modzitama kuti, “Ngati ndi ndewu ndili wokonzeka koma zakuti nkhunizi ndizisiya
ndiye muyiwale. Munthu wopanda mphamvu ngati iwe sungamalimbane ndi ine ayi.
Sukudzimvera chisoni?”

Podziwa kuti sakadatha kuwayanjanitsa, anthu ena adatsanzika kuti iwo akupita kumudzi. A
Moya adanena modzitamandira kuti anthuwo akapita kumudziko akawauze akazi awo a Fatsani
kuti afufutidwa. Adati, ngati satulukira adzawayang’ane kumunda kwawoko. Ine ndilibe
chibwana. Mukungofuna kunditengetsa tsoka apa.”

A Fatsani adayankha moleza mtima kuti, “Wakufa sadziwika.” Inu mukupita kumudziko
mukangowafotokozera za mkanganowu basi. Mukanene kuti chomwe chinatsitsa dzaye ndi
mtengo wa m’munda mwanga. Awa asadzitame chifukwa wofufuta mnzake sanadziwike.”

“Ukuti chiyani iwe? Makani amenewa ukukuchititsa ndi ufiti kapena chiyani? Kuonda konseko
ungamenye munthu? Kapenatu ukufuna ndingokukhalira?” Apa n’kuti a Moya atagwira a
Fatsani pakhosi.

Nthawi yosakhalitsa chindewu chadzaoneni chidagundika. A Moya amati akaponya chibakera, a

Fatsani achizinda, kudali kumenya mphepo osati munthu. Mnzawo amene amamuderera uja
ndiye adayima nazo zibakera zomwe zidawaonetsa nyenyezi masanasana. Ndewu ya a Moya
idali yapakamwa chabe.

Anthu omwe adali kuonerera ndewuyo adawasiya osawalanditsa kwa mphindi zingapo kuti
ayambe aonetsana mbwadza. Makamaka adachita dala kuti a Moya azindikire kuti sibwino
kutsogoza mawu. Opambana pa ndewu ngakhalenso pa mpikisano wa mtundu wina uliwonse
amadziwika pomaliza pa ndewuyo kapena mpikisanowo. Apa a Moya adatsimikizadi kuti ‘
wakufa sadziwika.” Adasasanthidwa kwambiri ndi bambo Fatsani womwe sanawaganizire kuti
n’kuwaumbudza.

(Jhango Chichewa Bukhu la Fomu 4)

7
DZINA: _________________________________ SUKULU: ___________________________

MAFUNSO

(i) Kodi ndi ndani adayambitsa mkangano m’nkhaniyi?

_____________________________________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) N’chifukwa chiyani anthu akutchulidwa m’nkhaniyi adayambana?
_____________________________________________________________________
(Malikisi 2)
(iii) Tchulani makhalidwe awiri a bambo Fatsani.
_____________________________________________________________________
__________________________________________________________(Malikisi 2)
(iv) Fotokozani kufunika kumodzi kololerana pakati pa anthu.
_____________________________________________________________________
(Malikisi 2)
(v) Perekani chifukwa chimene a Moya amaganiza kuti akhoza kuumbudza a Fatsani.
_____________________________________________________________________
__________________________________________________________(Malikisi 2)
(vi) Tsimikizani mawu oti ‘wakufa sadziwika’ malingana ndi nkhani mwawerengayi.
_____________________________________________________________________
__________________________________________________________(Malikisi 2)
(vii) Pezani matanthauzo a mawu otsatirawa omwe ali m’nkhaniyi.
a. Nkhambakamwa_____________________________________ (Malikisi 1)
b. Kufufuta___________________________________________ (Malikisi 1)
c. Kupala moto kudambwe_______________________________ (Malikisi 1)
d. Posafuna kusisima____________________________________ (Malikisi 1)
(viii) Kodi mikuluwiko yotsatirayi ikutanthauzanji malingana ndi nkhani mwawerengayi:
a. Mwamuna mnzako m’pachulu
__________________________________________________________________
_______________________________________________________ (Malikisi 2)
b. Chomwe chidautsa mapiri pa chigwa
__________________________________________________________________
_______________________________________________________ (Malikisi 2)

8
DZINA: _________________________________ SUKULU: ___________________________

ix. Pezani mawu otsutsana ndi mawu oti “kudzichepetsa” mnkhaniyi.

_____________________________________________________________________

(Malikisi 1)

Gawo C (Malikisi 15)

Chifupikitso

6. Werengani nkhani yotsatirayi mosamala. Ili ndi mawu 139 ndipo muyifupikitse kuti ikhale

ndi mawu osachepera 45 koma asapitirire 55.

MALONDA

Malonda ndi msintho wa zinthu. Kale malonda amachitika pongosinthana zinthu. Mwachitsanzo,
ngati wina ali ndi nkhuku ndipo akufuna chimanga, ofuna chimanga uja amapeza wina amene
akufuna nkhukuyo ndipo amasinthana naye.

Malonda otere adatha masiku ano. Masiku ano tikati malonda , munthu amaganizira za ndalama
basi. Kupita kumsika opanda ndalama, ndiye kuti sugula kanthu.

Malondawa amachitikira malo osiyanasiyana. Ena amachitikira m’misika yokhazikika, ena

yoyendayenda m’mbali mwa msewu ndipo ena amayendayenda m’makomo. Malo ochitira
malonda onsewa ali ndi ubwino ndi kuyipa kwake. Malonda oyendayenda m’makomo ndi
abwino chifukwa amathandiza ogula kuti asayende mtunda wautali ndi kutaya nthawi yawo
kukasaka katundu yemwe akufuna. Ngakhale zili choncho, nthawi zambiri ogula amakhala alibe
mwayi wosankha katundu yemwe akadakhala naye ngati akadapita kumsika komwe kumakhala
zinthu zambiri. Malondawa kawirkawiri amakhalanso okwera mtengo.

Kwa ogulitsa malondawa ndi abwino nthawi zina chifukwa amatha kupeza phindu lochuluka pa
zinthu zawo. Komabe poti masiku sakoma onse, nthawi zina ogulitsawa amalirira ku utsi poona
kuti atha kuyenda tsiku lonse koma osagulitsa.

9
DZINA: _________________________________ SUKULU: ___________________________

______________________________________________________________________________

Gawo D (Malikisi 15)

Chimasuliro

7. Masulirani nkhani yotsatirayi m’chichewa chomveka bwino.

CONSERVING ENVIRONMENT

Wildlife is a source of economy in Malawi. It is a backbone of tourism sector. Tourists from

Western countries have been visiting Mulanje Mountain in order to see Mulanje cedar.
Others proceed to Lengwe National Park to see black rhinoceros.

We need to report poaching cases in protected areas to authorities like Malawi Police
Service and Department of Parks and Wildlife. Poaching is illegal and it leads to extinction
of essential species in this country. Poachers kill elephants and extract ivories and export

10
DZINA: _________________________________ SUKULU: ___________________________

them.

_________________________________________________________________________

MAFUNSO ATHERA PANO

11

You might also like